Malawi News

Opikisana pa mpando wa utsogoleri wa dziko asanamizire kuti Mulungu waatuma – Chaima

M’modzi mwa olankhulapo pa nkhani za ndale ndi ulamuliro wabwino, George Chaima wati onse amene akudzapikisana nawo pa mpando wa mtsogoleri wa dziko, asamanamizile kuti atumidwa ndi Mulungu, ponena kuti ngati atumidwa ndi Mulungu akuyenera akwele mapiri kupemphera kuti Malawi akhale ndi mtsogoleri wabwino koma asalowe nawo ndale.


A Chaima ati kuchuluka kwa atsogoleri opikisana omwe pano akwana kale khumi ndi atatu (13) ndi chisonyezo cha dyera lomwe andalewa alinalo lofuna kupeza phindu pa dziko la Malawi.


Iwo ati kumanamizira Mulungu chifukwa choti tonse sitikumuwona ndi kumfunsa mwa chindunji ndi kumulakwira Mulungu chifukwa atsogoleri ena ananenapo kuti atumidwa ndi Mulungu koma athera kuzunza aMalawi ndi kuwononga dziko kotheratu.


“Aliyense amene akuti wayitanidwa ndi Mulungu adzipita kukalalikira m’makwalala ndi m’mizinda kuti atsogoleri a ndale ozuza aMalawi mulungu awachotse ayike atsogoleri abwino,” anatero a Chaima.


A Chaima anena izi pomwe amatsilira ndemanga mawu a m’modzi mwa omwe akupikisana nawo pa mpando wa mtsogoleri wa dziko a Smart Swira omwe ati iwo atumidwa ndi mulungu kuti awombole Malawi.


Poyankhula mu pologalamu ya Kulinji pa wayilesi ya Times, a Swira ati iwo ngakhale akuyima pawokha koma Mulungu adzawapambanitsa masankho a pa 16 September kuposa theka la mavoti onse.


Bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) lati kufikira pa 20 June, atsogoleri okwana 13 ndi omwe atenga zikalata ndi kupeleka ndalama yokwana 10 million Kwacha zomwe ndi zina mwa ndondomeko zofunika munthu amene akufuna kudzapikisana nawo pa mpando wa mtsogoleri wa dziko lino.


Atsogoleri anayi omwe ndi a Smart Swira, Hardwick Kaliya, Adil James Chilungo ndi a Milward Tobias ndi ena omwe atenga kale zikalata Koma oti adzayima pawokha pa masankho ndipo ena onse ali ndi zipani zomwe akudziyimilira.